17 Pakuti Kristu sanandituma ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Kristu ungayesedwe wopanda pace.
18 Pakuti mau a mtanda ali ndithu cinthu copusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tirikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.
19 Pakuti kulembedwa,Ndidzaononga nzeru za anzeru,Ndi kucenjerakwa ocenjera odidzakutha.
20 Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitsa nzeru ya dziko lapansi?
21 Pakuti popeza m'nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yace, silinadziwa Mulungu, cidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirawo mwa copusa ca kulalikira.
22 Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikilo, ndi Ahelene atsata nzeru:
23 koma ife tilalikira Kristu wopacikidwa, kwa Ayudatu cokhumudwitsa, ndi kwa amitundu cinthu copusa;