16 Koma akaoneka wina ngati wotetana, tiribe makhalidwe otere, kapena ife, kapena Eklesia wa Mulungu.
17 Koma pakulalikira ici sinditama inu, popeza simusonkhanira cokoma, koma coipa.
18 Pakutitu poyamba posonkhana inu mu Mpingo, ndimva kuti pakhala malekano mwa inu; ndipo ndibvomereza penapo.
19 Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo obvomerezedwa aonetsedwemwa inu.
20 Cifukwa cace, pakusonkhana inu pamodzi sikutheka kudya mgonero wa Ambuye;
21 pakuti pakudyaku yense athanga watenga mgonero wace wa yekha, ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera.
22 Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Eklesia wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena ciani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m'menemo? Sindikutamani.