2 Mudziwa kuti pamene munali amitundu, munatengedwa kunka kwa mafano aja osalankhula, monga munatsogozedwa.
3 Cifukwa cace ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yew ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.
4 Ndipo pali mphatso zosiyana, koma Mzimu yemweyo.
5 Ndipo pali mautumiki osiyana, koma Ambuye yemweyo.
6 Ndipo pali macitidwe osiyana, koma Mulungu yemweyo, wakucita zinthu zonse mwa onse.
7 Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao.
8 Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzace mau a cidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo: