39 Nyama yonse siiri imodzimodzi; koma yinandi Ya anthu, ndi yina ndiyo nyama ya zoweta, ndi yina ndiyo nyama ya mbalame, ndi yina ya nsomba.
40 Palinso matupi am'mwamba, ndi matupi apadziko: koma ulemerero wa lam'mwamba ndi wina, ndi ulemerero wa lapadziko ndi winanso.
41 Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi m'ulemerero.
42 9 Comweconso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m'cibvundi, liukitsidwa m'cisabvundi;
43 10 lifesedwa m'mnyozo, liukitsidwa m'ulemerero; lifesedwa m'cifoko, liukitsidwa mumphamvu;
44 lifesedwa thupi Iacibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi Iacibadwidwe, palinso lauzimu.
45 Koteronso kwalembedwa, 11 Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. 12 Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.