6 Ndinanka ine, anathirira Apolo; kama Mulungu anakulitsa.
7 Cotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; kama Mulungu amene akulitsa.
8 Koma wookayo ndi wothirirayoali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yace ya iye yekha, monga mwa kucititsa kwace kwa iye yekha.
9 Pakuti ife ndife anchito anzace a Mulungu; cilimo ca Mulungu, cimango ca Mulungu ndi inu.
10 Monga mwa cisomo ca Mulungu cidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo amangira pamenepo.
11 Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Kristu.
12 Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golidi, siliva, miyala va mtengo wace, mtengo, maudzu, dziputu,