1 PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu, mwa cifuniro ca Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali m'Akaya lonse:
2 Cisomo kwa inu ndi mtendere zocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.
3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa citonthozo conse,
4 woo titonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iri yonse, mwa citonthozo cimene titonthozedwa naco tokha ndi Mulungu.
5 Pakuti monga masautso a Kristu aticurukira ife, coteronso citonthozo cathu cicuruka mwa Kristu,