14 monganso munatibvomerezera ife pena, kuti ife ndife kudzitamandira kwanu, monga momwe inunso muli kudzitamandira kwathu m'tsiku la Ambuye wathu Yesu.
15 Ndipo m'kulimbika kumene ndinafuna kudza kwa inu kale, kuti mukakhalenaco cisomo caciwiri;
16 ndipo popyola kwanu kupita ku Makedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Makedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya.
17 Pamenepo, pakufuna cimene, kodi ndinacitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima kodi ndizitsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, eya, ndi iai, iai?
18 Koma Mulungu ali wokhulupirika, kuti mau athu a kwa inu sanakhala eya ndi iai.
19 Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silvano ndi Timoteo) sanakhala eya ndi iai, koma anakhala eya mwa iye.
20 Pakuti monga mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa iye eya; cifukwa cacenso ali mwa iye Amen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.