15 Cifukwa cace sikuli kanthu kwakukuru ngatinso atumiki ace adzionetsa monga atumiki a cilungamo; amene cimariziro cao cidzakhala monga nchito zao.
16 Ndinenanso, Munthu asandiyese wopanda nzeru; koma ngati mutero, mundilandirenso ine monga wopanda nzeru, kuti inenso ndidzitamandire pang'ono.
17 Cimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m'kulimbika kumene kwa kudzitamandira.
18 Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira.
19 Pakuti mulolana nao opanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru inu nokha.
20 Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope.
21 Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofoka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.