18 Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira.
19 Pakuti mulolana nao opanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru inu nokha.
20 Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope.
21 Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofoka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.
22 Kodi ali Ahebri? Inenso. Kodi ali Aisrayeli? Inenso. Kodi ali mbeu ya Abrahamu? Inenso.
23 Kodi ali atumiki a Kristu? (ndilankhula monga moyaruka), makamaka ine; m'zibvutitso mocurukira, m'ndende mocurukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawiri kawiri.
24 Kwa Ayuda ndinalandirakasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi.