21 Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofoka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.
22 Kodi ali Ahebri? Inenso. Kodi ali Aisrayeli? Inenso. Kodi ali mbeu ya Abrahamu? Inenso.
23 Kodi ali atumiki a Kristu? (ndilankhula monga moyaruka), makamaka ine; m'zibvutitso mocurukira, m'ndende mocurukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawiri kawiri.
24 Kwa Ayuda ndinalandirakasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi.
25 Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka combo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;
26 paulendo kawiri kawiri, moopsya mwace mwa mitsinje, moopsya mwace mwa olanda, 1 moopsya modzera kwa mtundu wanga, moopsya modzera kwa amitundu, moopsya m'mudzi, moopsya m'cipululu, moopsya m'nyanja, moopsya mwaabale onyenga;
27 m'cibvutitso ndi m'colemetsa, m'madikiro kawiri kawiri, 2 m'njala ndi ludzu, m'masalo a cakudyakawiri kawiri, m'cisanu ndi umarisece.