8 Kuti ngakhale ndakumvetsani cisoni ndi kalata uja, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata uja anakumvetsani cisoni, ngakhale kwa nthawi yokha.
9 Tsopano ndikondwera, sikuti mwangomvedwa cisoni, koma kuti mwamvetsedwa cisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m'kanthu kali konse.
10 Pakuti cisoni ca kwa Mulungu citembenuzira mtima kueipulumutso, cosamvetsanso cisoni; koma cisonicadziko lapansi cicita imfa.
11 Pakuti, taonani, ici comwe, cakuti mudamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, khama lalikuru lanji cidalicita mwa inu, komanso codzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso cangu, komanso kubwezera cilango! M'zonse muoadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo.
12 Cifukwa cace ndingakhale ndalembera kwa inu, sindinacita cifukwa ca iye amene anacita coipa, kapena cifukwa ca iye amene anacitidwa coipa, koma kuti khama lanu la kwa ife lionetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu.
13 Cifukwa ca icitatonthozedwa; ndipo m'citonthozo cathu tinakondwera koposa ndithu pa cimwemwe ca Tito, kuti mzimu wace unatsitsimutsidwa ndi inu nonse.
14 Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye cifukwa ca inu, sindinamvetsedwa manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'coonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala coonadi.