25 Nadzautsa mphamvu yace ndi mtima wace ayambane ndi mfumu ya kumwela ndi khamu lalikuru la nkhondo; ndi mfumu ya kumwela ndi khamu lalikuru ndi lamphamvu ndithu; koma sadzaimika, popeza adzamlingiririra ziwembu.
26 Inde iwo akudyako cakudya cace adzamuononga; ndi ankhondo ace adzasefukira, nadzagwaambiri ophedwa.
27 Ndipo mafumu awa onse awiri mitima yao idzakumbuka kucita zoipa, nadzanena bodza ali pa gome limodzi; koma osapindula nalo; pakuti kutha kwace kudzakhala pa nthawi yoikika.
28 Ndipo adzabwerera ku dziko lace ndi cuma cambiri; ndi mtima wace udzatsutsana ndi cipangano copatulika, nadzacita cifuniro cace, ndi kubwerera ku dziko lace.
29 Pa nthawi yoikika adzabwera, nadzalowa kumwela; koma sikudzakhala monga nthawi yoyamba ija, kapena yotsirizayi.
30 Pakuti zombo za ku Kitimu zidzafika kuyambana naye; cifukwa cace adzatenga nkhawa, nadzabwerera, nadzaipidwa mtima ndi cipangano copatulika, nadzacita cifuniro cace; adzabweranso, nadzasamalira otaya cipangano copatulika.
31 Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lace; nadzacotsa nsembe yosalekezayo, nadzaimitsa conyansa copululutsaco.