32 Ndipo akucitira coipa cipanganoco iye adzawaipsa, ndi kuwasyasyalika; koma anthu akudziwa Mulungu wao adzalimbika mtima, nadzacita mwamphamvu.
33 Ndipo aphunzitsi a anthu adzalangiza ambiri, koma adzagwa ndi lupanga, ndi lawi lamoto, ndi undende, ndi kufunkhidwa masiku ambiri.
34 Ndipo pakugwa iwo adzathandizidwa ndi thandizo laling'ono; koma ambiri adzaphatikizana nao ndi mau osyasyalika.
35 Nadzagwa aphunzitsi ena kuwayesa ndi moto, ndi kuwatsutsa, ndi kuwayeretsa, mpaka nthawi ya citsiriziro; pakuti kukaliko kufikira nthawi yoikika.
36 Ndipo mfumu idzacita monga mwa cifuniro cace, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iri yonse nidzanena zodabwiza pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzacitidwa ukaliwo; pakuti cotsimikizika m'mtimaco cidzacitika.
37 Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ace, kapena coikhumba akazi, kapena kusamalira milungu iri yonse; pakuti idzadzikuza koposa onse.
38 Koma kumalo kwace idzacitira ulemu mulungu wa malinga; ndi mulungu amene makolo ace sanaudziwa, adzaulemekeza ndi golidi, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wace, ndi zinthu zofunika.