10 Nanena naonso, Mukani mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lace iye amene sanamkonze ratu kanthu; cifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamacita cisoni; pakuti cimwemwe ca Yehova ndico mphamvu yanu.
11 Ndipo Alevi anatontholetsa anthu onse, ndi kuti, Khalani muli cete; pakuti lero ndi lopatulika; musamacita cisoni.
12 Napita anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukuru; popeza anazindikira mau amene adawafotokozera.
13 Ndipo m'mawa mwace akuru a nyumba za makolo a anthu onse, ansembe, ndi Alevi anasonkhana pamodzi kwa Ezara mlembi, kuti atole nzeru za mau a cilamulo.
14 Napeza munalembedwa m'cilamulo kuti Yehova analamulira ndi Mose, kuti ana a Israyeli azikhala m'misasa pa madyerero a mwezi wacisanu ndi ciwiri,
15 ndi kuti azilalikira ndi kumveketsa m'midzi mwao monse ndi m'Yerusalemu, ndi kuti, Muziturukira kuphiri, ndi kutengako nthambi za azitona, ndi nthambi za mitengo yamafuta, ndi nthambi za mitengo yamcisu, ndi zinkhwamba za migwalangwa, ndi nthambi za mitengo zothonana, kumanga nazo misasa monga munalembedwa.
16 Naturuka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yace, ndi m'mabwalo ao, ndi m'mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la cipata ca kumadzi, ndi pa khwalala la cipata ca Efraimu.