22 Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikilo, ndi Ahelene atsata nzeru:
23 koma ife tilalikira Kristu wopacikidwa, kwa Ayudatu cokhumudwitsa, ndi kwa amitundu cinthu copusa;
24 koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Ahelene, Kristu 1 mphamvu ya Mulungu, ndi 2 nzeru ya Mulungu.
25 Cifukwa kuti copusa ca Mulungu ciposa anthu ndi nzeru zao; ndipo cofoka ca Mulunguciposa anthu ndi mphamvu yao.
26 Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti 3 saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iai;
27 koma 4 Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akacititse manyazi anzeru; ndipo zofoka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akacititse manyazi zamphamvu;
28 ndipo zopanda pace za dziko lapansi, ndi zonyozeka, anazisankhula Mulungu, ndi zinthu zoti kulibe; 5 kuti akathere zinthu zoti ziriko;