3 Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu comangirira ndi colimbikitsa, ndi cosangalatsa,
4 Iye wakulankhula lilime, adzimangirira yekha, koma iye wakunenera amangirira Mpingo.
5 Ndipo ndifuna inu nonse mula'nkhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire comangirira.
6 Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikaku, pindulitsani ciani, ngati sindilankhui landi inu kapena m'bvumbulutso, kapena m'cidziwitso, kapena m'cinenero, kapena m'ciphunzitsot
7 Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mau, ngati toliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa maliridwe, cidzazindikirikabwanji cimene ciombedwa kapena kuyimbidwa?
8 Pakuti ngad Lipenga lipereka mao osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo?
9 Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mau omveka bwino, kudzazindikirika bwanji cimene cilankhulidwa? Pakuti mudzakhala olankhula kumlengalenga.