5 Ndipo ndifuna inu nonse mula'nkhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire comangirira.
6 Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikaku, pindulitsani ciani, ngati sindilankhui landi inu kapena m'bvumbulutso, kapena m'cidziwitso, kapena m'cinenero, kapena m'ciphunzitsot
7 Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mau, ngati toliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa maliridwe, cidzazindikirikabwanji cimene ciombedwa kapena kuyimbidwa?
8 Pakuti ngad Lipenga lipereka mao osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo?
9 Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mau omveka bwino, kudzazindikirika bwanji cimene cilankhulidwa? Pakuti mudzakhala olankhula kumlengalenga.
10 Iripo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau pa dziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau.
11 Cifukwa cace, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwaine.