24 Yense, m'mene anaitanidwamo, abate, akhale momwemo ndi Mulungu.
25 Koma kunena za anamwali, ndiribe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani coyesa ine, monga wolandira cifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika.
26 Cifukwa cace ndiyesa kuti ici ndi cokoma cifukwa ca cibvuto ca nyengo yino, kuti nkwabwino kwa munthu kukhala monga ali.
27 Kodi wamangika kwa mkazi? Usafune kumasuka. Kodi wamasuka kwa mkazi? Usafune mkazi.
28 Koma ungakhale ukwatira, sunacimwa; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanacimwa. Koma otere adzakhala naco cisautso m'thupi, ndipo ndikulekani.
29 Koma ici nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nao akazi akhalebe monga ngati alibe;
30 ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu;