1 Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: Tidziwa kuti tid naco cidziwitso tonse. Cidziwitso citukumula, koma cikondicimangirira.
2 Ngati wina ayesa kuti adziwa kanthu sanayambe kudziwa monga ayenera kudziwa.
3 Koma ngati wina akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi iye.
4 Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano siliri kanthu pa dziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi.
5 Pakuti ngakhalenso iriko yoti yonenedwa milungu, kapena m'mwamba, kapena pa dziko lapansi, monga iriko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri;
6 koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zicokera kwa iye, ndi ire kufikira kwa iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Kristu, amene zinthu zonse ziri mwa iye, ndi ife mwa iye.
7 Komatu cidziwitso siciri mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo cikumbu mtima cao, popeza ncofoka, cidetsedwa.