8 Koma cakudya sicitibvomerezetsa kwa Mulungu; kapena ngati sitidya sitisowa; kapena ngati tidya tiribe kupindulako,
9 Koma yang'anirani kuti ulamuliro wanu umene ungakhale cokhumudwitsa ofokawo.
10 Pakuti wina akaona iwe amene uli naco cidziwitso, ulikukhala pacakudya m'kacisi wa fano, kodi cikumbu mtima cace, popeza ali wofoka, sieidzalimbika kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano?
11 Pakuti mwa cidziwitso cako wofokayo atayika, ndiye mbale amene Kristu anamfera.
12 Koma pakucimwira abale, ndi kulasa cikumbu mtima cao cofoka, mucimwira kotero Kristu.
13 Cifukwa cace, ngati cakudya cikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya ayama ku nthawi yonse, kuti ndiogakhumudwitse mbale wanga.