1 Mwenzi mutandilola pang'ono ndi copusaco! Komanso mundilole.
2 Pakuti ndicita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Kristu.
3 Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kucenjerera kwace, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima ziri kwa Kristu.
4 Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikira, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandira, kapena uthenga wabwino wa mtundu wina umene simunalandira, mulolana nave bwino lomwe.
5 Pakuti ndiyesa kuti sindinaperewera konse ndi atumwi oposatu,