25 Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa cinsinsi ici, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israyeli, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;
26 ndipo cotero Israyeli yense adzapulumuka; monganso kunalembedwa, kuti,Adzaturuka ku Ziyoni Mpulumutsi;Iye adzacotsa zamwano kwa Yakobo:
27 Ndipo ici ndi cipangano canga ndi iwo,Pamene ndidzacotsa macimo ao.
28 Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ali ngati adani, cifukwa ca inu; koma kunena za cisankhidwe, z ali okondedwa, cifukwa ca makolo.
29 Pakuti 1 mphatso zace ndi kuitana kwace kwa Mulungu sizilapika.
30 Pakuti 2 monga inunso kale simunamvera Mulungu, koma tsopano mwalandira cifundo mwa kusamvera kwao,
31 coteronso iwo sanamvera tsopano, kuti iwonso akalandire cifundo, cifukwa ca cifundo ca kwa inu.