1 Ndipo iye amene ali wofoka m'cikhulupiriro, mumlandire, koma si kucita naye makani otsutsana ai.
2 Munthu mmodzi akhulupirira kuti adye zinthu zonse, koma wina wofoka angodya zitsamba.
3 Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wakudyayo; pakuti Mulungu wamlandira.
4 Ndani iwe wakuweruza mnyamata wa mwini wace? iye aimirira kapena kugwa kwa mbuye wace wa mwini yekha. Ndipo adzaimiritsidwa; pakuti Ambuye ali wamphamvu kumuimiritsa.
5 Munthu wina aganizira kuti tsiku lina liposa linzace; wina aganizira kuti masiku onse alingana. Munthu ali yense akhazikike konse mumtima mwace.