28 Koma pamene ndikatsiriza ici, ndi kuwasindikizira iwo cipatso ici, ndidzapyola kwanu kupita ku Spanya.
29 Ndipo 4 ndidziwa kuti pamene ndikadza kwanu, ndidzafika m'kudzaza kwace kwa cidalitso ca Kristu.
30 Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi cikondi ca Mzimu, kuti 5 mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu cifukwa ca ine;
31 kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima;
32 6 kuti ndi cimwemwe ndikadze kwa inu mwa cifuno ca Mulungu, ndi kupumula pamodzi ndi inu.
33 Ndipo 7 Mulungu wa mtendere akhale ndi inu nonse. Amen.