3 Pakuti Kristunso sanadzikondweretsa yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakuoyoza iwe Inagwa pa Ine,
4 Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa cipiriro ndi citonthozo ca malembo, tikhale ndi ciyembekezo.
5 Ndipo Mulungu wa cipiriro ndi wa citonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzace, monga mwa Kristu Yesu;
6 kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu.
7 Cifukwa cace mulandirane wina ndi mnzace, monganso Kristu anakulandirani inu, kukacitira Mulungu ulemerero.
8 Ndipo ndinena kuti Kristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, cifukwa ca coonadi ca Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo,
9 ndi kuti anthu a mitundu yina akalemekeze Mulungu, cifukwa ca cifundo; monga kwalembedwa,Cifukwa ca icindidzakubvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu,Ndidzayimbira dzina lanu.