1 Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wamkazi wa Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkreya;
2 kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zili zonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.
3 Mulankhule Priska ndi Akula, anchito anzanga m'Kristu Yesu,
4 amene anapereka khosi lao cifukwa ca moyo wanga; amene ndiwayamika, si ine ndekha, komanso Mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu;