16 Mulankhulane wina ndi mnzace ndi kupsompsona kopatulika. Mipingo yonse ya Kristu ikulankhulani inu.
17 Ndipo ndikudandaulirani; abale, yang'anirani iwo akucita zopatutsana ndi zopunthwitsa, kosalingana ndi ciphunzitsoco munaciphunzira inu; ndipopotolokani pa iwo.
18 Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Kristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asoceretsamitiina ya osalakwa.
19 Pakuti kumvera kwanu kunabuka kwa anthu onse. Cifukwa cace ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pa zabwino, koma ozungulidwa pa zoipa.
20 Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanva: Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino.Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi inu nonse.
21 Timoteo wanchito mnzanga akulankhulani inu; ndi Lukiyo ndi Yasoni ndi Sosipatro, abale anga.
22 Ine Tertio, ndirikulemba kalata ameneyu, ndikulankhulani inu mwa Ambuye.