2 kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zili zonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.
3 Mulankhule Priska ndi Akula, anchito anzanga m'Kristu Yesu,
4 amene anapereka khosi lao cifukwa ca moyo wanga; amene ndiwayamika, si ine ndekha, komanso Mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu;
5 ndipo mulankhule Mpingo wa Ambuye wa m'nyumba mwao. Mulankhule Epeneto wokondedwa wanga, ndiye cipatso coundukula ca Asiya ca kwa Kristu,
6 Mulankhule Mariya amene anadzilemetsa ndi nchito zambiri zothandiza inu.
7 Mulankhule Androniko ndi Yuniya, anansi anga, ndi andende anzanga, amene ali omveka mwa amitumwi, amenenso ananditsogolera ine mwa Kristu.
8 Mulankhule Ampliato wokondedwa wanga mwa Ambuye.