3 Ndipo uganiza kodi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akucita zotere, ndipo uzicitanso iwe mwini, kuti udzapulumuka pa mlandu wit Mulungu?
4 Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wace, ndi cilekerero ndi cipiriro cace, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?
5 Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa dzuwa la mkwiyo ndi la kubvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;
6 amene adzabwezera munthu ali yense kolingana ndi nchito zace;
7 kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi cisaonongeko, mwa kupirira pa nchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha;
8 koma kwa iwo andeu, ndi osamvera coonadi, koma amvera cosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi kuzaza,
9 nsautso ndi kuwawa mtima, kwa moyo wa munthu ali yense wakucita zoipa, kuyambira Myuda, komanso Mhelene;