1 Ndipo potero Myuda aposa Dinji? Kapena mdulidwe upindulanji?
2 Zambiri monse monse: coyamba, kuti mau a Mulungu anaperekedwa kwa iwo.
3 Nanga bwanji ngati ena sanakhulupira? Kodi kusakhulupira kwao kuyesa cabe cikhulupiriko ca Mulungu?
4 Msatero ai. Koma Mulungu akhale woona, ndimo anthu onse akhale onama; monga kwalembedwa,Kuti Inu mukayesedwe wolungama m'maneno anu,Ndi kuti mukalakike m'mene muweruzidwa.
5 Koma ngati cosalungama cathu citsimikiza cilungamo ca Mulungu, tidzatani ife? Kodi ali wosalungama Mulungu, amene afikitsa mkwiyo? (ndilankhula umo anenera munthu).
6 Msatero ai. Ngati kotero, Mulungu adzaweruza bwanji mlandu wa dziko lapansi?