13 M'mero mwao muli manda apululu;Ndi lilime lao amanyenga; Ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao;
14 M'kamwa mwao mudzala ndi zotemberera ndi zowawa;
15 Miyendo yao icita liwiro kukhetsa mwazi;
16 Kusakaza ndi kusauka kuli m'njira zao;
17 Ndipo njira ya mtendere sanaidziwa;
18 Kumuopa Mulungu kulibe pamaso pao.
19 Ndipo tidziwa kuti zinthu ziri zonse cizinena cilamulo cizilankhulira iwo ali naco cilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;