5 Koma ngati cosalungama cathu citsimikiza cilungamo ca Mulungu, tidzatani ife? Kodi ali wosalungama Mulungu, amene afikitsa mkwiyo? (ndilankhula umo anenera munthu).
6 Msatero ai. Ngati kotero, Mulungu adzaweruza bwanji mlandu wa dziko lapansi?
7 Pakuti ngati coonadi ca Mulungu cicurukitsa ulemerero wacecifukwa ca bodza langa, nanga inenso ndiweruzidwa bwanji monga wocimwa?
8 Ndipo tilekerenji kunena, Ticite zoipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama.
9 Ndipo ciani tsono? kodi tiposa ife? Iai ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Ahelene omwe, kuti onsewa agwidwa ndi ucimo;
10 monga kwalembedwa,Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi;
11 Palibe mmodzi wakudziwitsa, Palibe mmodzi wakuloodola Mulungu;