1 Ndipo tsono tidzanena kuti Abrahamu, kholo lathu monga mwa thupi, analandira ciani?
2 Pakuti ngati Abrahamu anayesedwa wolungama cifukwa ca nchito, iye akhala naco codzitamandira; koma kulinga kwa Mulungu ai.
3 Pakuti lembo litani? Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo cinawerengedwa kwa iye cilungamo,
4 Ndipo kwa iye amene agwira nchito, mphotho siiwerengedwa ya cisomo koma ya mangawa.
5 Koma kwa iye amene sacita, koma akhulupirira iye amene ayesa osapembedza ngati olungama, cikhulupiriro cace ciwerengedwa cilungamo.