15 Ndipo ciani tsono? Tidzacimwa kodi cifukwa sitiri a lamulo, koma a cisomo? Msatero ai.
16 Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ace akumvera iye, mukhalatu akapolo ace a yemweyo mulikumvera iye; kapena a ucimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kucilungamo?
17 Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a ucimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a ciphunzitso cimene munaperekedweraco;
18 ndipo pamene munamasulidwa kuucimo, munakhala akapolo a cilungamo,
19 Ndilankhula manenedwe a anthu, cifukwa ca kufoka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a conyansa ndi a kusayeruzika kuti zicite kusayeruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a cilungamo kuti zicite ciyeretso.
20 Pakuti pamene inu munali aka polo a ucimo, munali osatumikira cilungamo.
21 Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu zimene mucita nazo manyazi tsopano? pakuti cimariziro ca zinthu izi ciri imfa.