2 Msatero ai. Ife amene tiri akufa ku ucimo, tidzakhala bwanji cikhalire m'menemo?
3 Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace?
4 Cifukwa cace tinaikldwa m'manda pamodzi ndi iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Kristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, cotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.
5 Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi iye m'cifanizidwe ca imfa yace, koteronso tidzakhala m'cifani'Zidwe ca kuuka kwace;
6 podziwa ici, kuti umunthu wathu wakale unapacikidwa pamodzi ndi iye, kuti thupilo la ucimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a ucimo;
7 pakuti iye amene anafa anamasulidwa kuucimo.
8 Koma ngati ife tinafa ndi Kristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi iye;