1 Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.
2 Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo la ucimo ndi la imfa.
3 Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita, popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo m'thupi;
4 kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.