15 Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate,
16 Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu;
17 ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye.
18 Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.
19 Pakuti ciyembekezetso ca colengedwa cilimilia bvumbulutso la ana a Molungu.
20 Pakuti colengedwaco cagonietsedwa kuutsiru, cosafuna mwini, koma cifukwa ca iye amene anacigonjetsa,
21 ndi ciyembekezo kuti colengedwa comwe cidzamasulidwa ku ukapolo wa cibvundi, ndi kolowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu,