3 Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita, popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo m'thupi;
4 kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.
5 Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu:
6 pakuti cisamaliro ca thupi ciri imfa; koma cisamaliro ca mzimu ciri moyo ndi mtendere.
7 Cifukwa cisamaliro ca thupi cidana ndi Mulungu; pakuti sicigonja ku cilamulo ca Mulungu, pakuti sicikhoza kutero.
8 Ndipo iwo amene ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.
9 Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wace wa Kristu.