11 pakuti anawo asanabadwe, kapena asanacite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si cifukwa ca nchito ai, koma cifukwa ca wakuitanayo,
12 cotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkuru adzakhala kapolo wa wamng'ono.
13 Inde monga kunalembedwa, Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.
14 Ndipo tsono tidzatani? Kodi ciripo cosalungama ndi Mulungu? Msatero ai.
15 Pakuti anati ndi Mose, Ndidzacitira cifundo amene ndimcitira cifundo, ndipo ndidzakhala ndi cisoni kwa iye amene ndikhala naye cisoni.
16 Cotero sicifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene acitira cifundo.
17 Pakuti lembo linena kwa Farao, Cifukwa ca ici, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe pa dziko lonse lapansi.