24 ndi ife amenenso iye anatiitana, si a mwa Ayuda okha okha, komanso a mwa anthu amitundu?
25 Monga atinso mwa Hoseya,Amene sanakhala anthu anga, ndidzawacha anthu anga;Ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa.
26 1 Ndipo kudzali, kuti pamalo pamenepo kunanenedwa kwa iwo, Simuli anthu anga ai,Pomwepo iwo adzachedwa ana a Mulungu wamoyo.
27 Ndipo Yesaya apfuula za Israyeli, kuti,2 Ungakhale unyinji wa ana a Israyeli ukhala monga mcenga wa kunyanja, 3 cotsalira ndico cidzapulumuka.
28 Pakuti Ambuye adzacita mau ace pa dziko lapansi, kuwatsiriza mwacidule.
29 Ndipo monga Yesaya anati kale,4 Ngati Ambuye wa makamu a kumwamba sanatisiyira ife mbeu,Tikadakhala monga Sodoma, ndipo tikadafanana ndi Gomora.
30 Cifukwa cace tidzatani? 5 Kuti amitundu amene sanatsata cilungamo, anafikira cilungamo, ndico cilungamo ca cikhulupiriro;