1 Ndipo polowanso Iye m'Kapernao atapita masiku ena, kunamveka kuti ali m'nyumba.
2 Ndipo ambiri anaunjikana, kotero kuti anasowa malo, ngakhale pakhomo pomwe; ndipo analankhula nao mau.
3 Ndipo anadza kwa Iye otenga munthu wodwala manjenje, wonyamulidwa ndi anthu anai.
4 Ndipo pamene sanakhoza kufika kuli Iye, cifukwa ca khamu la anthu, anasasula chindwi pokhala Iye; ndipo pamene anatha kuliboola, anatsitsa mphasa m'mene alinkugonamo wodwala manjenjeyo,
5 Ndipo Yesu pakuona cikhulupiriro cao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, macimo ako akhululukidwa.
6 Koma anakhalapo ena a alembi akuganizira mumtima mwao,
7 Munthu amene atero bwanji? acita mwano; akhoza ndani kukhululukira macimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu?