Marko 10 BL92

Asasiyane mwamuna ndi mkazi wace

1 Ndipo ananyamuka Iye kumeneko, nadza ku maiko a ku Yudeya ndi ku tsidya lija la Yordano; ndipo anasonkhananso kwa Iye makamu a anthu; ndipo monga anazolowera, anawaphunzitsanso.

2 Ndipo anadza kwa Iye Afarisi, namfunsa Iye ngati kuloledwa kuti munthu acotse mkazi wace, namuyesa Iye.

3 Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi Mose anakulamulirani ciani?

4 Ndipo anati, Mose analola kulembera kalata wakulekanira, ndi kumcotsa.

5 Koma Yesu anati kwa iwo, Cifukwa ca kuuma kwa mitima yanu anakulemberani lamulo ili.

6 Koma kuyambira pa ciyambi ca malengedwe anawapanga mwamuna ndi mkazi.

7 Cifukwa cace mwamuna adzasiya atate wace ndi amai wace, ndipo adzaphatikizana ndi mkazi wace;

8 ndipo awiriwa adzakhala thupi limodzi: kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi.

9 Cifukwa cace cimene Mulungu anacimanga pamodzi, asacilekanitse munthu.

10 Ndipo m'nyumba ophunzira anamfunsanso za cinthu ici.

11 Ndipo Iye ananena nao, Munthu ali yense akacotsa mkazi wace, nakakwatira wina, acita cigololo kulakwira mkaziyo;

12 ndipo ngati mkazi akacotsa mwamuna wace, nakwatiwa ndi wina, acita cigololo iyeyu.

Yesu adalitsa tiana

13 Ndipo analinkudza nato kwa Iye tiana, kuti akatikhudze; ndipo ophunzirawo anawadzudzula.

14 Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.

15 Ndithu ndinena ndi inu, Munthu ali yense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.

16 Ndipo Iye anatiyangata, natidalitsa, ndi kuika manja ace pa ito.

Mnyamata mwini cuma cambiri

17 Ndipo pamene Iye anaturuka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzacita ciani kuti ndilandire moyo wosatha?

18 Ndipo Yesu anati kwa iye, Undicha Ine wabwino bwanji? palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu.

19 Udziwa malamulo: Usaphe, Usacite cigololo, Usabe, Usacite umboni wakunama, Usanyenge, Lemekeza atate wako ndi amako.

20 Ndipo iye anati kwa Iye, Mphunzitsi, zonsezi ndinazisunga kuyambira ndiri mwana.

21 Ndipo Yesu anamyang'ana, namkonda, nati kwa iye, Cinthu cimodzi cikusowa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo cuma udzakhala naco m'mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.

22 Koma nkhope yace inagwa pa mau awa, ndipo anacoka iye wacisoni; pakuti anali mwini cuma cambiri.

23 Ndipo Yesu anaunguzaunguza, nanena ndi ophunzira ace, Okhala naco cuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu ndi kubvuta nanga!

24 Ndipo ophunzirawo anazizwa ndithu ndi mau ace. Koma Yesu anayankhanso nanena nao, Ananu, nkobvuta ndithu kwa iwo akutama cuma kulowa mu Ufumu wa Mulungu!

25 Nkwa pafupi kuti ngamila ipyole diso la singano koposa kuti mwini cuma alowe mu Ufumu wa Mulungu.

26 Ndipo anadabwa, nanena kwa Iye, Ndipo angathe kupulumuka ndani?

27 Yesu anawayang'ana iwo nati, Sikutheka ndi anthu, koma kutheka ndi Mulungu; pakuti zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.

28 Petro anayamba kunena naye, Onani, ife tinasiya zonse, ndipo tinakutsatani Inu.

29 Yesu anati, Ndinena ndi inu ndithu, Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda, cifukwa ca Ine, ndi cifukwa ca Uthenga Wabwinowo,

30 amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthawi yino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amai, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthawi irinkudza, moyo wosatha.

31 Koma ambiri akuyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.

Ali panjira kukwera ku Yerusalemu. Ana a Zebedayo apempha ulemu

32 Ndipo iwo anali m'njira alinkukwera kunka ku Yerusalemu; ndipo Yesu analikuwatsogolera; ndipo iwo anazizwa; ndipo akumtsatawo anacita mantha. Ndipo Iye anatenganso khumi ndi awiriwo, nayamba kuwauza zinthu zimene zidzamfikira Iye,

33 nati, Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akuru ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu;

34 ndipo adzamnyoza Iye, nadzamthira malobvu, nadzamkwapula Iye, nadzamupha; ndipo pofika masiku atatu adzauka.

35 Ndipo anadza kwa Iye Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, nanena naye, Mphunzitsi, tifuna kuti mudzaticitire cimene ciri conse tidzapempha kwa Inu.

36 Ndipo Iye anati kwa iwo, Mufuna kuti ndidzakucitireni inu ciani?

37 Ndipo iwo anati kwa Iye, Mutipatse ife kuti tikhale mmodzi ku dzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, m'ulemerero wanu.

38 Koma Yesu anati kwa iwo, Simudziwa cimene mucipempha, Mukhoza kodi kumwera cikho cimene ndimwera Ine? kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine?

39 Ndipo anati kwa Iye, Tikhoza. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Cikho cimene ndimwera Ine mudzamwera; ndipo ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine, mudzabatizidwa nao;

40 koma kukhala ku dzanja langa lamanja, kapena kulamanzere sikuli kwanga kupatsa; koma kuli kwa iwo amene adawakonzeratu,

41 Ndipo pamene khumiwo anamva, anayamba kupsa mtima cifukwa ca Yakobo ndi Yohane.

42 Ndipo Yesu anawaitana, nanena nao, Mudziwa kuti iwo amene ayesedwa ambuye a mitundu ya anthu amacita ufumu pa iwo; ndipo akuru ao amacita ulamuliro pa iwo.

43 Koma mwa inu sikutero ai; kama amene ali yense afuna kukhala wamkuru mwa inu adzakhala mtumiki wanu;

44 ndipo amene ali yense afuna kukhala woyamba mwa inu adzakhala kapolo wa onse.

45 Pakuti ndithu, Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wace dipo la kwa anthu ambiri.

Bartimeyu wakhungu wa ku Yeriko

46 Ndipo iwo anafika ku Yeriko; ndipo m'mene Iye analikuturuka m'Yeriko, ndi ophunzira ace, ndi khamu lalikuru la anthu, mwana wa Timeyu, Bartimeyu, wopempha wakhungu, analikukhala pansi m'mbali mwa njira.

47 Ndipo pamene anamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, anayamba kupfuula, ndi kunena, Yesu, Inu Mwana wa Davide, mundicitire ine cifundo.

48 Ndipo ambiri anamuyamula kuti atonthole: koma makamaka anapfuulitsa kuti, Inu Mwana wa Davide, mundicitire cifundo.

49 Ndipo Yesu anaima, nati, Mwitaneni. Ndipo anaitana wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka, akuitana.

50 Ndipo iye anataya copfunda cace, nazunzuka, nadza kwa Yesu.

51 Ndipo Yesu anamyankha, nati, Ufuna kuti ndikucitire ciani? Ndipo wakhunguyo anati kwa Iye, Raboni, ndilandire kuona kwanga.

52 Ndipo Yesu anati kwa iye, Muka; cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso; namtsata Iye panjira.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16