Marko 8 BL92

Yesu acurukitsa mikate kaciwiri

1 Masiku ajawo pakukhalanso khamu lalikuru la anthu, ndipo analibe kanthu kakudya, iye anadziitanira ophunzira ace, nanena nao,

2 Ndimva nalo cifundo khamulo, cifukwa ali ndi Ine cikhalire masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya:

3 ndipo ngati ndiwauza iwo amuke kwao osadya kanthu, adzakomoka panjira; ndipo ena iwo acokera kutali.

4 Ndipo ophunzira ace anamyankha Iye, kuti, Munthu adzatha kutenga kuti mikate yakukhutitsa anthu awa m'cipululu muno?

5 Ndipo anawafunsa, Muli nayo mikate ingati? Ndipo anati, Isanu ndi iwiri.

6 Ndipo analamulira anthu a khamulo akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa ophunzira ace, kuti apereke kwa iwo; ndipo anapereka kwa khamulo.

7 Ndipo anali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anatidalitsa, nati atipereke itonso.

8 Ndipo anadya nakhuta; ndipo anatola makombo malicero asanu ndi awiri.

9 Ndipo iwo anali ngati zikwi zinai; ndipo Iye analawirana nao.

10 Ndipo pomwepo analowa m'ngaiawa ndi akhupunzira ace, nafika ku mbali ya ku Dalmanuta.

Afarisi afuna cizindikilo

11 Ndipo Afarisi anaturuka, nayamba kufunsana naye, ndi kufuna kwa Iye cizindikilo cocokera Kumwamba, namuyesa Iye.

12 Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wace, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna cizindikilo bwanji? indetu ndinena kwa inu, ngati cizindikilo cidzapatsidwa kwa mbadwo uno!

13 Ndipo anawasiya iwo, nalowanso m'ngalawa, nacoka kunka ku tsidya lija.

Cotupitsa mkate ca Afarisi

14 Ndipo ophunzira adaiwala kutenga mikate, ndipo analibe mkate m'ngalawa koma umodzi wokha.

15 Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang'anirani, penyani kuti mupewe cotupitsa mkate ca Afarisi, ndi cotupitsa mkate ca Herode.

16 Ndipo anatsutsana wina ndi mnzace, nanena kuti, Tiribe mikate.

17 Ndipo Yesu pamene anazindikira, ananena nao, Bwanji mutsutsana cifukwa mulibe mkate? kodi kufikira tsopano simuzindikira, nisimudziwitsa? kodi muli nayo mitima yanu youma?

18 Pokhala nao maso simupenya kodi? ndi pokhala nao makutu simukumva kodi? ndipo simukumbukila kodi?

19 Pamene ndinawagawira anthu zikwi zisanu mikate isanu ija, munatola mitanga ingati yodzala ndi makombo? Ananena naye, Khumi ndi iwiri.

20 Ndipo mikate isanu ndi iwiri kwa anthu zikwi zinai, munatola malicero angati odzala ndi makombo? Ndipo ananena naye, Asanu ndi awiri.

21 Ndipo Iye ananena nao, Simudziwitsa ngakhale tsopano kodi?

Yesu aciritsa munthu wakhungu ku Betsaida

22 Ndipo anadza ku Betsaida. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze.

23 Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, naturukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malobvu m'maso mwace, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi?

24 Ndipo anakweza maso, nanena, Ndiona anthu; pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo.

25 Pamenepo anaikanso manja m'maso mwace; ndipo anapenyetsa, naciritsidwa, naona zonse mbee.

26 Ndipo anamtumiza amuke kwao, nanena, Usalowe konse m'mudzi.

Petro abvomereza Kristu

27 Ndipo anaturuka Yesu, ndi ophunzira ace, nalowa ku midzi ya ku Kaisareya wa Filipi; ndipo panjira anafunsa ophunzira ace, nanena nao, Kodi anthu anena kuti Ine ndine yani?

28 Ndipo ananena, nati, Yohane Mbatizi; ndi ena, Eliya; koma ena, Mmodzi wa aneneri.

29 Ndipo Iye anawafunsa, Koma inu munena kuti ndine yani? Petro anayankha nanena naye, Ndinu Kristu.

30 Ndipo anawauzitsa iwo kuti asanene kwa munthu mmodzi za Iye.

31 Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akuru ndi ansembe akulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkuca wace akauke.

32 Ndipo mauwo ananena poyera. Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula.

33 Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ace, namdzudzula Petro, nanena, Coka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.

Kunyamula mtanda

34 Ndipo anadziitanira khamulo la anthu pamodzi ndi ophunzira ace, nati kwa iwo, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wace, nanditsate Ine.

35 Pakuti yense wakufuna kupulumutsa moyo wace adzautaya; ndipo yense wakutaya moyo wace cifukwa ca Ine, ndi cifukwa ca Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa.

36 Pakuti munthu apindulanji akadzilemezera dziko lonse, natayapo moyo wace?

37 Pakuti munthu akapereka ciani cosintha naco moyo wace?

38 Pakuti yense wakucita manyazi cifukwa ca Ine, ndi ca mau anga mu mbadwo uno wacigololo ndi wocimwa, Mwana wa munthu adzacitanso manyazi cifukwa ca iyeyu, pamene Iye adzafika nao angelo ace oyera, mu ulemerero wa Atate wace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16