Marko 6 BL92

Apeputsa Yesu ku Nazarete

1 Ndipo Iye anaturuka kumeneko; nafika ku dziko la kwao; ndipo ophunzira ace anamtsata.

2 Ndipo pofika dzuwa la Sabata, anayamba kuphunzitsa m'sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zocitidwa ndi manja ace?

3 Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Mariya, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yuda, ndi Simoni? Ndipo alongo ace sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.

4 Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m'dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ace, ndi m'nyumba yace.

5 Ndipo kumeneko sanakhoza Iye kucita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja ace pa anthu odwala owerengeka, nawaciritsa.

6 Ndipo anazizwa cifukwa ca kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.

Yesu atuma khumi ndi awiriwo

7 Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza Iwo awiri awiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa;

8 ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena thumba, kapena ndalama m'lamba lao;

9 koma abvale nsapato; ndipo anati, Musabvale malaya awiri.

10 Ndipo ananena nao, Kumene kuli konse mukalowa m'nyumba, khalani komweko kufikira mukacokako.

11 Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakucoka kumeneko, sansani pfumbi liri ku mapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo.

12 Ndipo anaturuka nalalikira kuti anthu atembenuke mitima.

13 Ndipo anaturutsa mizimu yoipa yambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri akudwala, nawaciritsa.

Kuphedwa kwa Yohane Mbatizi

14 Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lace lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo cifukwa cace mphamvu izi zicitacita mwa Iye.

15 Koma ena ananena, kuti, Ndiye Eliya, Anati enanso, Ndiye mneneri, monga ngati mmodzi wa aneneriwo,

16 Koma Herode pamene anamva, ananena, Yohane amene ndamdula mutu, wauka iyeyo.

17 Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m'nyumba yandende, cifukwa ca Herodiya, mkazi wa Filipo mbale wace; cifukwa adamkwatira iye.

18 Pakuti Yohane adanena kwa Herode, Si kuloledwa kwa inu kukhala naye mkazi wa mbale wanu.

19 Ndipo Herodiya anamuda, nafuna kumupha; koma sanakhoza;

20 pakuti Herode anaopa Yohane, podziwa kuti ali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo anamsunga iye. Ndipo pamene anamva iye anathedwa nzeru, oakondwa kumva iye.

21 Ndipo pamene panafika tsiku loyenera, tsiku la kubadwa kwace kwa Herode, iye anawakonzera phwando akuru ace ndi akazembe ace ndi anthu omveka a ku Galileya;

22 ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiya analowa yekha nabvina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pacakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine ciri conse ucifuna, ndidzakupatsa iwe.

23 Ndipo anamlumbirira iye, kuti, Ciri conse ukandipempha ndidzakupatsa, kungakhale kukugawira ufumu wanga.

24 Ndipo anaturuka, nati kwa amace, Ndidzapempha ciani? Ndipo iyel anati, Mutu wace wa Yohane Mbatizi.

25 Ndipo pomwepo analowa m'mangu m'mangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wace wa Yohane Mbatizi mumbizi.

26 Ndipo mfumu inamva cisoni cacikuru; koma cifukwa ca malumbiro ace, ndi ca iwo akukhala pacakudya, sanafuna kumkaniza.

27 Ndipo pomwepo mfumu inatuma mnyamata, namlamulira akatenge mutu wace; ndipo iye anamuka namdula mutu m'nyumba yandende;

28 natengera mutu wace mumbizi, naupereka kwa buthulo; ndipo buthu linaupereka kwa amace.

29 Ndipo m'mene ophunzira ace anamva, anadza nanyamula mtembo wace nauika m'manda.

Yesu acurukitsa mikate

30 Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza ziri zonse adazicita, ndi zonse adaziphunzitsa,

31 Ndipo Iye ananena nao, Idzani inu nokha padera ku malo acipululu, mupumule kamphindi, Pakuti akudza ndi akucoka anali piringu piringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya.

32 Ndipo anacokera m'ngalawa kunka ku malo acipululu padera.

33 Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikila, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ocokera m'midzi monse, nawapitirira.

34 Ndipo anaturuka Iye, naona khamu lalikuru la anthu, nagwidwa cifundo ndi iwo, cifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.

35 Ndipo pamene dzuwa lidapendeka ndithu, anadza kwa Iye ophunzira ace, nanena, Malo ana nga cipululu, ndi dzuwa lapendeka ndithu;

36 muwauze kuti amuke, alowe kumiraga ndi ku midzi yozungulira, akadzigulire okha kanthu kakudya.

37 Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya?

38 Ndipo Iye ananena nao, kuti, Muli nayo mikate ingati? pitani, mukaone. Ndipo m'mene anadziwa ananena, lsanu, ndi nsomba ziwiri.

39 Ndipo anawalamulira kuti akhalitse pansi onse magulu magulu pamsipu.

40 Ndipo anakhala pansi mabungwe mabungwe a makumi khumi, ndi a makumi asanu.

41 Ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang'anakumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri anagawira onsewo.

42 Ndipo anadya iwo onse, nakhuta.

43 Ndipo anatola makombo mitanga khumi ndi iwiri, ndiponso za nsomba.

44 Ndipo amene anadya mikate iyo anali amuna zikwi zisanu.

Yesu ayenda pa nyanja

45 Ndipo pomwepo Iye anakangamiza ophunzira ace alowe rri'ngalawa, ndi kumtsogolera kutsidya lija ku Betsaida, m'mene Iye yekha alimkuuza khamulo kuti amuke.

46 Ndipo atalawirana nao, anacoka Iye, nalowa m'phiri kukapemphera,

47 Ndipo pofika madzulo ngalawa inali pakati pa nyanja, ndi Iye yekha pamtunda.

48 Ndipo pakuwaona ali kubvutidwa ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nao, pa uionda wacinai wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire;

49 koma iwo, pamene anamuona alikuyenda panyanja, anayesa kuti ndi mzukwa, napfuula:

50 pakuti iwo onse anamuona Iye, nanthunthumira. Koma pomwepo anawalankhula nanena nao, Limbani mtima; ndinetu, musaope,

51 Ndipo Iye anakwera, nalowa kwa iwo m'ngalawa, ndipo mphepo inaleka; ndipo anadabwa kwakukuru mwa iwo okha;

52 pakuti sanazindikira za mikateyo, kama mitima yao inauma.

53 Ndipo ataoloka iwo, anafika pamtunda ku Genesarete, nakoceza padooko.

54 Ndipo pamene anaturuka m'ngalawa anamzindikila pomwepo,

55 nathamangira dziko lonselo nayamba kunyamula anthu odwaia pa akama ao, kufika nao kumene anamva kuti analiko Iye.

56 Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena m'miraga, anthu anagoneka odwala pamisika, 1 nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya cobvala cace; ndipo onse amene anamkhudza anaciritsidwa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16