Marko 13 BL92

Yesu aneneratu za masautso alinkudza

1 Ndipo pamene analikuturuka Iye m'Kacisi, mmodzi wa ophunzira ace ananena kwa Iye, Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba yotere.

2 Ndipo Yesu anati kwa iye, Kodi waona nyumba izi zazikuru? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzace, umene sudzagwetsedwa.

3 Ndipo pamene anakhala Iye pa phiri la Azitona, popenyana ndi Kacisi, anamfunsa Iye m'tseri Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Andreya, kuti,

4 Tiuzeni, zinthu izi zidzacitika liti? Ndi cotani cizindikilo cace cakuti ziri pafupi pa kumarizidwa zinthu izi zonse?

5 Ndipo Yesu anayamba kunena nao, Yang'anirani kuti munthu asakusoceretseni.

6 Ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Iye; nadzasoceretsa ambiri.

7 Ndipo m'mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zace za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenerakucitika izi; koma sicinafike cimariziro.

8 Pakuti mtundu wa anthu udzayambana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu unzace: padzakhaia zibvomezi m'malo m'malo; padzakhala njala; izi ndi zoyambira za zowawa.

9 Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu kwa akuru a mirandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafwnu mudzaimirira cifukwa ca Ine, kukhale umboni kwa iwo.

10 Ndipo Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.

11 Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musada nkhawa usanayambe mrandu ndi cimene mudzalankhula; koma ci mene cidzapatsidwa kwa inu m'mphindi yomweyo, mucilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera.

12 Ndipo mbale adzapereka mbale wace kuti amuphe, ndi atate mwana wace; ndi ana adza yambana ndi akuwabala, nadzawaphetsa,

13 Ndipo adzada inu anthu onse cifukwa ca dzina langa: koma iye wakupirira kufikira cimariziro, yemweyo adzapulumutsidwa.

Yesu aneneratu za cisautso cacikuru

14 Ndipo pamene mukaona conyansa ca kupululutsa cirikuima pomwe siciyenera (wakuwerenga azindikile), pamenepo a m'Yudeya athawire kumapiri;

15 ndi iye amene ali pamwamba pa chindwi asatsike, kapena asalowe kukaturutsa kanthu m'nyumba mwace;

16 ndi iye amene ali kumunda asabwere kudzatenga Malaya ace.

17 Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana masiku awol

18 Ndipo pempherani kuti kusakhale m'nyengo yacisanu.

19 Pakuti masiku aja padzakhala cisautso, conga sicinakhala cinzace kuyambira ciyambi ca cilengedwe cimene Mulungu anacilenga ndi kufikira tsopano, ndipo sicidzakhalanso nthawi zonse.

20 Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense; koma cifukwa ca osankhidwa amene anawasankha, anafupikitsa masikuwo.

21 Ndipo pamenepo wina akati kwa inu, Onani Kristu ali pano; kapena, Onani, uko; musabvomereze;

22 pakuti adzauka Akristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzacita zizindikilo ndi zozizwitsa, kuti akasoceretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe.

23 Koma yanganirani; onani ndakuuziranitu zinthu zonse, zisanafike.

Yesu aneneratu kuti adzabwera

24 Koma m'masikuwo, citatha cisautso cimeneco, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzapatsa kuunika kwace,

25 ndi nyenyezi zidzagwa kucokera m'mwamba ndi mphamvu ziri m'mwamba zidzagwedezeka.

26 Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa munthu alinkudza m'mitambo ndi mphamvu yaikuru, ndi ulemerero.

27 Ndipo pamenepo adzatuma angelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ace ocokera ku mphepo zinai, kuyambira ku malekezero ace a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.

28 Ndipo phunzirani ndi mkuyu fanizo lace; pamene pafika kuti nthambi yace ikhala yanthete, ndipo anaphuka masamba ace, muzindikira kuti layandikira dzinja;

29 comweco inunso, pamene muona zinthu izi zirikucitika, zindikirani kuti ali pafupi pakhomo.

30 Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapita kufikira zinthu izi zonse zitacitika.

31 Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.

32 Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yace sadziwa munthu, angakhale angelo m'Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye.

Za kulindirira

33 Yang'anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yace.

34 Monga ngati munthu wa paulendo, adacoka kunyumba kwace, nawapatsa akapolo ace ulamuliro, kwa munthu ali yense nchito yace, nalamulira wapakhomo adikire.

35 Cifukwa cace dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yace yakubwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pausiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa;

36 kuti angabwere balamantha nakakupezani muli m'tulo.

37 Ndipo cimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16