1 Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri la Azitona, anatuma awiri a ophunzira ace,
2 nanena nao, Mukani, lowani m'mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa buru womangidwa, amene palibe munthu anakhalapo kale lonse; mmasuleni, ndipo mubwere naye.
3 Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Katini, Ambuye amfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno.
4 Ndipo anacoka, napeza mwana wa buru womangidwa pakhomo, pabwalo m'khwalala, nammasula iye.
5 Ndipo ena akuima kumeneko ananena nao, Mucita ciani ndi kumasula mwana wa buru?
6 Ndipo anati kwa iwo monga momwe ananena Yesu: ndipo anawalola iwo apite naye.
7 Ndipo anabwera naye mwana wa buru kwa Yesu, naika zobvala zao pa iye, ndipo Iye anakhala pamenepo.
8 Ndimo ambiri anayala zobvala zao panjira; ndi ena zitsamba, anazidula m'minda.
9 Ndipo akutsogolera, ndi iwo akutsata, anapfuula, Hosana; Wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye:
10 Wolemekezeka Ufumu ulinkudza, wa atate wathu Davide; Hosana m'Kumwamba-mwamba.
11 Ndipo Iye analowa m'Yerusalemu, m'Kacisi; ndipo m'mene anaunguza zinthu zonse, popeza ndi madzulo, anaturuka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwoo.
12 Ndipo m'mawa mwace, ataturuka ku Betaniya, Iye anamva njala.
13 Ndipo anaona mkuyu kutali, uli ndi masamba; ndipo anadza Iye, kuti kapena akapezapo kanthu: ndipo m'mene anafikako anapeza palibe kanthu koma masamba okha; pakuti siinali nyengo yace ya nkhuyu.
14 Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ace anamva,
15 Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa m'Kacisi, nayamba kuturutsa akugulitsa ndi akugula malonda m'Kacisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando yaogulitsa nkhunda;
16 ndipo sanalola munthu ali yense kunyamula cotengera kupyola pakati pa Kacisi.
17 Ndipo anaphunzitsa, nanena nao, Sicilembedwa kodi, Nyumba yanga idzachedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? koma inu mwaiyesa phanga la acifwamba.
18 Ndipo ansembe akuru ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, cifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi ciphunzitso cace.
19 Ndipo masiku onse madzulo anaturuka Iye m'mudzi.
20 Ndipo m'mene anapitapo m'mawa mwace, anaona kuti mkuyu uja unafota, kuyambira kumizu.
21 Ndipo Petro anakumbukila, nanena naye, Rabi, onani, wafota mkuyuwo munautemberera.
22 Ndipo Yesu anayankha nanena nao, Khulupirirani Mulungu,
23 Ndithu ndinena ndi inu, kuti, Munthu ali yense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja; wosakayika mumtima mwace, koma adzakhulupirira kuti cimene acinena cicitidwa, adzakhala naco.
24 Cifukwa cace ndinena ndi inu, Zinthu ziri zonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.
25 Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, kholulukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhulolukire inu zolakwa zanu.
27 Ndipo iwo anadzanso ku Yerusalemu; ndipo m'mene Iye anali kuyenda m'Kacisi, anafika kwa Iye ansembe akuru, ndi alembi ndi akuru;
28 nanena naye, Izi muzicita ndi ulamuliro wotani? Kapena anakupatsani ndani ulamuliro uwu wakucita izi?
29 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani mau amodzi, mundiyankhe Ine, ndipo ndidzakuuzani ulamuliro umene ndicita nao zinthu zimenezi.
30 Ubatizo wa Yohane ucokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu? Mundiyankhe.
31 Ndipo anatsutsana mwa iwo okha, nanena, Tikati, Kumwamba; adzanena iye, Ndipo simunakhulupirira iye bwanji?
32 Koma tikati, Kwa anthu —anaopa anthuwo; pakuti onse anamuyesa Yohane mneneri ndithu.
33 Ndipo iwo anamyankha Yesu, nanena, Sitidziwa. Ndipo Yesu ananena nao, Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndicita nao zinthu zimenezi.