Marko 5 BL92

Yesu aciritsa wogwidwa ndi mzimu wonyansa ku Gerasa

1 Ndipo anafika tsidya lina la nyanja, ku dziko la Agerasa,

2 Ndipo pameneadaturuka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu woturuka kumanda wa mzimu wonyansa,

3 amene anayesa nyumba yace kumanda; ndipo palibe munthu anakhoza kummanganso, inde ngakhale ndi unyolo;

4 pakuti adafomangidwa kawiri kawiri ndi matangadza ndimaunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya.

5 Ndipo masiku onse, usiku ndi usana, anakhala m'manda ndi m'mapiri, napfuula, nadzitematema ndi miyala.

6 Ndipo pakuona Yesu kutali, anathamanga, namgwadira Iye;

7 ndipo anapfuula ndi mau olimba, nanena, Ndiri ndi ciani ine ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkurukuru? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze.

8 Pakuti ananena kwa iye, Turuka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu.

9 Ndipo anamfunsa, Dzina lako ndani? Ndipo ananena kwa Iye, Dzina langa ndine Legio; cifukwa tiri ambiri.

10 Ndipo anampempha Iye kwambiri kuti asaiturutsire kunja kwace kwa dziko.

11 Ndipo panali pamenepo gulu lalikuru la nkhumba zirinkudya kuphiri.

12 Ndipo inampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo.

13 Ndipo anailolao Ndipo mizimu yonyansa inaturuka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja.

14 Ndipo akuziweta anathawa, nauza m'mudzi, ndi kwninda. Ndipo anadza kudzaona cocitikaco.

15 Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wobvala ndi wa nzeru zace zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo.

16 Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo anacitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo.

17 Ndipo anayamba kumpempha Iye kuti acoke m'malire ao,

18 Ndipo m'mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye.

19 Ndipo sanamlola, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikuru anakucitira Ambuye, ndi kuti anakucitira cifundo.

20 Ndipo anamuka nayamba kulalikira ku Dekapoli zinthu zazikuru Yesu adamcitira iye; ndipo anthu onse anazizwa.

Mwana wa Yairo, Mkazi wokhudza copfunda ca Yesu

21 Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikuru linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja.

22 Ndipo anadzako mmodzi wa akuru a sunagoge, dzina lace Yairo; ndipo pakuona Iye, anagwada pa mapazi ace, nampempha kwambiri,

23 nanena, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalimkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti kapulwnuke, ndi kukhala ndi moyo.

24 Ndipo ananka naye pamodzi; ndipo khamu lalikuru linamtsata Iye, ndi kumkanikiza Iye.

25 Ndipo munthu wamkazi amene anali ndi nthenda yacidwalire zaka khwni ndi ziwiri,

26 ndipo anamva zowawa zambiri ndi asing'anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osacira pang'ono ponse, koma makamaka nthenda yace idakula,

27 m'mene iye anamva mbiri yace ya Yesu, anadza m'khamu kumbuyo kwace, nakhudza cobvala cace.

28 Pakuti ananena iye, Ngati ndikakhudza ngakhale zobvala zace ndidzapulumutsidwa.

29 Ndipo pomwepo kasupe wa nthenda yace adaphwa; ndipo anazindikira m'thupi kuti anaciritsidwa cibvutiko cace.

30 Ndipo pomwepo Yesu, pamene anazindikira mwa Iye yekha kuti mphamvu idaturuka mwa Iye, anapotoloka m'khamu, nanena, Ndani anakhudza zobvala zanga?

31 Ndipo ophunzira ace ananena kwa Iye, Muona kuti khamu lirikukanikiza Inu, ndipo munena kodi, Wandikhudza ndani?

32 Ndipo Iye anaunguza-unguza kumuona iye amene adacita ici,

33 Koma mkaziyo anacita mantha, ndi kunthunthumira, podziwa cimene anamcitira iye, nadza, namgwadira, namuuza coona conse.

34 Ndipo anati kwa iye, Mwana wamkaziwe, cikhulupiriro, cako cakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wocira cibvutiko cako.

35 M'mene iye ali cilankhulire, anafika a ku nyumba ya mkuru wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; ubvutiranjinso Mphunzitsi?

36 Koma Yesu wosasamala mau olankhulidwawo, ananena kwa mkuru wa sunagoge, Usaope, khulupirira kokha.

37 Ndipo sanalola munthu yense kutsagana naye, koma Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wace wa Yakobo.

38 Ndipo anafika ku nyumba kwace kwa mkuru wa sunagoge; ndipo anaona cipiringu, ndi ocita maliro, ndi akukuwa ambiri

39 Ndipo m'mene atalowa, ananena nao, Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafa, koma ali m'tulo.

40 Ndipo anamseka Iye pwepwete, Koma Iye anawaturutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amace, ndi ajawo anali naye, nalowa m'mene munali mwanayo.

41 Ndipo anagwira dzanja lace la mwana, nanena kwa iye, Talita koumi; ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe, Uka.

42 Ndipo pomwepo buthulo linauka, niliyenda; pakuti linali la zaka khumi ndi ziwiri. Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukuru.

43 Ndipo anawalamulira kwambiri kuti asadziwe ici munthu mmodzi, nawauza kuti ampatse iye kudya.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16