Marko 15 BL92

Yesu aweruzidwa ndi Pilato

1 Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe akuru, ndi akuru a anthu, ndi alembi, ndi akuru a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.

2 Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha, nanena naye, Mwatero.

3 Ndipo ansembe akuru anamnenera Iye zinthu zambiri.

4 Ndipo Pilato anamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? taona, akunenera Iwe zinthu zambiri zotere.

5 Koma Yesu sanayankhanso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa.

6 Ndipo adafuwamasulira paphwando wandende mmodzi, amene iwo anampempha,

7 Ndipo analipo wina dzina lace Baraba, womangidwa pamodzi ndi opanduka, amene anapha munthu mumphandumo.

8 Ndipo khamu la anthu anabwera nayamba kupempha kuti acite monga adafuwacitira.

9 Ndipo Pilato anawayankha, nanena nao, Kodi mufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayuda?

10 Pakuti anazindikira kuti ansembe akuru anampereka Iye mwanjiru.

11 Koma ansembe akuru anasonkezera khamulo, kuti makamaka awamasulire Baraba.

12 Ndipo Pilato anawayankhanso, nati kwa iwo, Pamenepo ndidzacita ciani ndi Iye amene mumchula Mfumu ya Ayuda?

13 Ndipo anapfuulanso, Mpacikeni pamtanda.

14 Ndipo Pilato ananena nao, Pakuti Iye anacita coipa cotani? Koma iwo anapfuulitsatu, Mpacikeni Iye.

15 Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Baraba, napereka Yesu, atamkwapula, akampacike pamtanda.

16 Ndipo asilikari anacoka naye nalowa m'bwalo, ndilo Pretorio; nasonkhanitsa gulu lao lonse.

17 Ndipo anambveka Iye cibakuwa, naluka korona waminga, nambveka pa Iye;

18 ndipo anayamba kumlankhula Iye, kuti, Tikuoneni, Mfumu ya Ayuda!

19 Ndipo anampanda Iye pamutu pace ndi bango, namthira malobvu, nampindira maondo, namlambira.

20 Ndipo atatha kumnyoza anambvula cibakuwaco nambveka Iye zobvala zace. Ndipo anaturuka naye kuti akampacike Iye pamtanda.

Ampacika Yesu pamtanda

21 Ndipo anakangamiza wina wopitirirapo, Simoni wa ku Kurene, alikucokera kuminda, atate wao wa Alesandere ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wace.

22 Ndipo anamtenga kunka naye ku malo Golgota, ndiwo, osandulika, Malo-a-bade.

23 Ndipo anampatsa vinyo wosanganiza ndi mure; koma Iye sanamlandira.

24 Ndipo anampacika Iye, nagawana zobvala zace mwa iwo okha, ndi kucita maere pa izo, kuti adziwe yense adzatengaciani.

25 Ndipo panali ora lacitatu, ndipo anampacika Iye.

26 Ndipo lembo la mlandu wace linalembedwa pamwamba, MFUMU YAAYUDA.

27 Ndipo anapacika pamodzi ndi Iye acifwamba awiri; mmodzi ku dzanja lace lamanja ndi wina kulamanzere.[

28 ]

29 Ndipo iwo akupitirirapo anamcitira mwano, napukusa mitu yao, nanena, Ha! iwe wakupasula Kacisi, ndi kummanga masiku atatu,

30 udzipulumutse mwini, nutsike pamtanda.

31 Moteronso ansembe akuru anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena, Anapulumutsa ena; sakhoza kudzipulumutsa yekha.

32 Atsike tsopano pamtanda, Kristu Mfumu ya Israyeli, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupacikidwa naye anamlalatira.

33 Ndipo pofika ora lacisanu ndi cimodzi, panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lacisanu ndi cinai.

34 Ndipo pa ora lacisanu ndi cinai Yesu anapfuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika,Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?

35 Ndipo ena akuimirirapo, paku mva, ananena, Taonani, aitana Eliya

36 Ndipo anathamanga wina, nadzaza cinkhupule ndi vinyo wosasa naciika pabango, namwetsa Iye nanena, Lekani; tione ngati Eliys adza kudzamtsitsa.

37 Ndipo Yesr anaturutsa mau okweza, napereka mzimu wace.

38 Ndipo cinsart cocinga ca m'Kacisi cinang'ambika pakati, kuyambira kumwamba kufikira pansi.

39 Ndipo pamene kenturiyo, woimirirapo popenyana ndi Iye, anaona kuti anapereka mzimu kotero, anati, Zoonadi, munthu uyu anali Mwana wa Mulungu.

40 Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang'anira kutali; mwa iwo anali Maliya wa Magadala, ndi Maliya amace wa Yakobo wamng'ono ndi wa Yose, ndi Salome;

41 amene anamtsata Iye, pamene anali m'Galileya, namtumikira; ndi akazi ena ambiri, amene anakwera kudza ndi Iye ku Yerusalemu.

Yesu aikidwa m'manda

42 Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzera, ndilo la pambuyo pa Sabata,

43 anadzapo Y osefe wa ku Arimateya, mkulu wa mirandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wace wa Yesu.

44 Ndipo Pilato anazizwa ngati adamwaliradi; naitana kenturiyo, namfunsa ngati adamwalira kale.

45 Ndipo pamene anacidziwa ndi kenturiyo, anamninkha Yosefe ntembowo.

46 Ndipo anagula oafuta, namtsitsa Iye, namkulunga n'bafutamo, namuika m'manda osenedwa m'thanthwe; nakunkhunicira mwala pa khomo la manda.

47 Ndipo Maliya wa Magadala ndi Maliya amace wa Yose anapenya pomwe anaikidwapo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16