Marko 9 BL92

Mawalitsidwe a Yesu paphiri

1 Ndipo ananena nao, Ndithu ndinena ndi inu kuti, Alipo ena akuimirira pano, amene sadzalawa imfa konse, kufikira akaona Ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu.

2 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nao pa phiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pao:

3 ndipo zobvala zace zinakhala zonyezimira, zoyera mbu; monga ngati muomba wotsuka nsaru pa dziko lapansi sangathe kuziyeretsai.

4 Ndipo anaonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, alikulankhulana ndi Yesu.

5 Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.

6 Pakuti sanadziwa cimene adzayankha; cifukwa anacita mantha ndithu.

7 Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mau munaturuka m'mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye.

8 Ndipo dzidzidzi pounguzaunguza, sanapenya munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni.

9 Ndipo pakutsika iwo paphiri, Iye anawalamulira kuti asauze munthu zinthu zimene adaziona, koma pamene Mwana wa munthu akadzauka kwa akufa ndipo.

10 Ndipo anasunga mauwo, nafunsana mwa iwo okha, kuti, Kuuka kwa akufa nciani?

11 Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Nanga alembi anena kuti adzayamba kufika Eliya?

12 Ndipo Iye ananena nao, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzakonza zinthu zonse; ndipo kwalembedwa bwanji za Mwana wa munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa cabe?

13 Koma ndinena ndi inu kuti anafikadi Eliya, ndipo anamcitiranso ziri zonse iwo anazifuna, monga kwalembedwa za iye.

Aciritsidwa mwana wogwidwa ndi mzimu wosalankhula

14 Ndipo pamene anadza kwa ophunzira, anaona khamu lalikuru la anthu ozungulira iwo, ndi alembi alikufunsana nao.

15 Ndipo pomwepo anthu onse a khamulo, pakumuona Iye, anazizwa kwambiri, namthamangira Iye, namlankhula.

16 Ndipo anawafunsa iwo, Mufunsa na nao ciani?

17 Ndipo wina wa m'khamulo anamyankha Iye, kuti, Mphunzitsi, ndadza naye kwa Inu mwana wanga, ali nao mzimu wosalankhula;

18 ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo acita thobvu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti auturutse; koma sanakhoza.

19 Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.

20 Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuona, pomwepo mzimuwo unamng'amba koopsya; ndipo anagwa pansi nabvimbvinika ndi kucita thobvu.

21 Ndipo Iye anafunsa atate wace, kuti, Cimeneci cinayamba kumgwira liti? Ndipo anati, Cidamyamba akali mwana.

22 Ndipo kawiri kawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kucita kanthu mtithandize, ndi kuticitira cifundo.

23 Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.

24 Pomwepo atate wa mwana anapfuula, nanena, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga.

25 Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lirikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, turuka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.

26 Ndipo pamene unapfuula, numng'ambitsa, unaturuka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira.

27 Koma Yesu anamgwira dzanja lace, namnyamutsa; ndipo anaimirira.

28 Ndipo pamene Iye adalowa m'nyumba, ophunzira ace anamfunsa m'tseri, kuti, Nanga bwanji sitinakhoza ife kuuturutsa?

29 Ndipo Iye anati kwa iwo, Mtundu uwu sukhoza kuturuka ndi kanthu kena konse, koma ndi kupemphera.

Wamkuru ndani m'Ufumu wa Mulungu

30 Ndipo anacoka iwo kumeneko, napyola pakati pa Galileya; ndipo Iye sanafuna kuti munthu adziwe.

31 Pakuti anaphunzitsa ophunzira ace, nanena nao, kuti, Mwana wa munthu aperekedwa m'manja a anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.

32 Koma iwo sanazindikira mauwo, naopa kumfunsa.

33 Ndipo iwo anadza ku Kapernao; ndipo pamene anakhala m'nyumba, Iye anawafunsa, Munalikutsutsana ninji panjira?

34 Koma iwo anakhala cete; pakuti anatsutsana wina ndi mnzace panjira, kuti, wamkuru ndani?

35 Ndipo m'mene anakhala pansi anaitana khumi ndi awiriwo; nanena nao, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse.

36 Ndipo anatenga kamwana, nakaika pakati pao, nakayangata, nanena nao,

37 Munthu ali yense adzalandira kamodzi ka tiana totere cifukwa ca dzina langa, alandira ine; ndipo yense amene akalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine.

Osatsutsana nafe athandizana nafe

38 Yohane anati kwa Iye, Mphunzitsi, tinaona munthu alikuturutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, cifukwa sanalikutsata ife.

39 Koma Yesu anati, Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzacita camphamvu m'dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera Ine zoipa.

40 Pakuti iye wosatsutsana ndi ife athandizana nafe.

41 Pakuti munthu ali yense adzakumwetsani inu cikho ca madzi m'dzina langa cifukwa muli ace a Kristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yace.

Malakwitso

42 Ndipo yense amene adzalakwitsa kamodzi ka tiana timeneto takukhulupirira Ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukuru wamphero ukolowekedwe m'khosi mwace, naponyedwe iye m'nyanja.

43 Ndipo ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: nkwabwino kwa iwe kulowa m'moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa m'gehena, m'moto wosazima.[

44 ]

45 Ndipo ngati phazi lako likulakwitsa, ulidule; kulowa iwe m'moyo wopunduka mwendo, kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi mapazi ako awiri ndi kuponyedwa m'gehena.[

46 ]

47 Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe m'Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa m'gehena;

48 kumeneko mphutsi yao siikufa, ndi mota suzimidwa.

49 Pakuti onse adzathiridwa mcere wamoto,

50 Mcere uli wabwino; koma ngati mcere unasukuluka, mudzaukoleretsa ndi ciani? Khalani nao mcere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16