1 Ndipo Iye anayamba kulankhula nao m'mafanizo. Munthu analima munda wamphesa, nauzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.
2 Ndipo m'nyengo yace anatuma kapolo kwa olimawo, kuti alandireko kwa olimawo zipatso za m'munda wamphesa.
3 Ndipo iwo anamtenga iye, nampanda, namcotsa wopanda kanthu.
4 Ndipo anatumanso kapolo wina kwa iwo; ndipo ameneyu anamlasa mutu, namcitira zomcititsa manyazi.
5 Ndipo anatuma wina; iyeyu anamupha; ndi ena ambiri; ena anawapanda, ndi ena anawapha.
6 Anamtsalira mmodzi, ndiye mwana wace wokondedwa; potsiriza anamtuma iye kwa iwo, nanena, Adzamcitira ulemu mwana wanga.
7 Koma olima ajawo, ananena mwa iwo okha, Ameneyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe iye, ndipo mundawu udzakhala wathu.
8 Ndipo anamtenga, namupha iye, namtaya kunja kwa munda.
9 Pamenepo mwini munda adzacita ciani? Adzafika, nadzaononga olimawo, nadzapereka mundawo kwa ena.
10 Kodi simunawerenga ngakhale lembo ili;Mwala umene anaukana omanga nyumba,Womwewu unayesedwa mutu wa pangondya:
11 Ici cinacokera kwa Ambuye, Ndipo ciri cozizwitsa m'maso mwathu?
12 Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nacoka.
13 Ndipo anatuma kwa Iye ena a Afarisi ndi a Aherode, kuti akamkole Iye m'kulankhula kwace.
14 Ndipo pamene anafika, ananena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo simusamala munthu; pakuti simuyang'ana nkhope ya anthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu moona: Nkuloleka kodi kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai?
15 Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye anadziwa cinyengo cao, nati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni rupiya latheka, kuti ndilione. Ndipo analitenga.
16 Ndipo ananena nao, Cithunzithunzi ici, ndi cilembo cace ziri za yani? Ndipo anati kwa Iye, Za Kaisara.
17 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Perekani zace za Kaisara kwa Kaisara, ndi zace za Mulungu kwa Mulungu. Ndipo anazizwa naye kwambiri.
18 Ndipo anadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa Iye, nanena,
19 Mphunzitsi, Mose anatilembera, kuti, Akafa mbale wace wa munthu, nasiya mkazi, wosasiyapo mwana, mbale wace atenge mkazi wace, namuuldtsire mbale waceyo mbeu.
20 Analipo abale asanu ndi awiri; woyamba anakwatira mkazi, nafa, wosasiya mbeu;
21 ndipo waciwiri anamkwatira, nafa, wosasiya mbeu; ndipo wacitatunso anatero momwemo;
22 ndipo asanu ndi awiriwo analibe kusiya mbeu. Potsiriza pace pa onse mkazinso anafa.
23 Pakuuka adzakhala mkazi wa yani wa iwowa? Pakuti asanu ndi awiriwo adamuyesa mkazi wao.
24 Yesu ananena nao, Simusocera nanga mwa ici, popeza mulibe kudziwa malembo, kapena mphamvu yace ya Mulungu?
25 Pakuti pamene adzauka kwa akufa, sakwatira, kapena sakwatiwa; koma akhala ngati angelo a Kumwamba. Koma za akufa, kuti akauldtsidwa;
26 simunawerenga m'kalata wa Mose kodi, za Citsambaco, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine Ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?
27 Sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: musocera inu ndithu.
28 Ndipo anadza mmodzi wa alembi, namva iwo alikufunsana pamodzi, ndipo pakudziwa kuti anawayankha bwino, anamfunsa Iye, Lamulo la m'tsogolo la onse ndi liti?
29 Yesu anayankha, kuti, La m'tsogolo ndili, Mvera, Israyeli; Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndiye mmodzi;
30 ndipouzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.
31 Laciwiri ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa.
32 Ndipo mlembiyo anati kwa Iye, Cabwino, Mphunzitsi, mwanena zoona kuti ndiye mmodzi; ndipo palibe wina, koma Iye:
33 ndipo, kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzace monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.
34 Ndipo palmona kuti anayankha ndi nzeru, Yesu anati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu analimbanso mtima kwnfunsa Iye kanthu.
35 Ndipo Yesu pamene anaphunzitsa m'Kacisi, anayankha, nanena, Bwanji alembi anena kuti Kristu ndiye mwana wa Davide?
36 Davide mwini yekha anati mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala ku dzanja langa lamanja, kufikira ndiwaika adani ako popondapo mapazi ako.
37 Davide mwini yekha amchula Iye Ambuye; ndipo ali mwana wace bwanji? Ndipo anthu a makamuwo anakondwa kumva Iye.
38 Ndipo m'ciphunzitso cace ananena, Yang'anirani mupewe alembi, akufuna kuyendayenda obvala miinjiro, ndi kulankhulidwa pamisika,
39 ndi kukhala nayo mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamapwando:
40 amenewo alusira nyumba za akazi amasiye, napemphera monyenga mau ambiri; amenewa adzalandira kulanga koposa.
41 Ndipo Iye anakhala pansi pandunji pa mosungiramo zopereka, napenya kuti khamu la anthu alikuponya ndalama mosungiramo; ndipo eni cuma ambiri anaponyamo zambiri.
42 Ndipo anadza mkazi wamasiye waumphawi, ndipo iye anaponyamo tindalama tiwiri tanng'ono tofa kakobiri kamodzi.
43 Ndipo anaitana ophunzira ace, nati kwa iwo, Ndithu ndinena ndi inu, Mkazi wamasiye amene waumphawi anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo:
44 pakuti anaponyamo onse mwa zocuruka zao; koma iye anaponya mwa kusowa kwace zonse anali nazo, inde moyo wace wonse.